June 27–July 3
MASALIMO 52-59
Nyimbo 38 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Umutulile Yehova Nkhawa Zako”: (Mph. 10)
Sal. 55:2, 4, 5, 16-18—Nthawi zina, Davide anali kukhala ndi nkhawa (w06 6/1 11 ndime 3 CN; w96 4/1 27 ndime 2 CN)
Sal. 55:12-14—Mwana wa Davide kuphatikizapo mnzake wa pamtima anamuukila (w96 4/1 30 ndime 1 CN)
Sal. 55:22—Davide anadalila thandizo la Yehova (w06 6/1 11 ndime 4 CN; w99 3/15 22-23 CN)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 56:8—Kodi mau akuti “sungani misozi yanga m’thumba lanu lacikopa” atanthauza ciani? (w09 6/1 29 ndime 1 CN; w08 10/1 26 ndime 3 CN)
Sal. 59:1, 2—Kodi zimene zinacitikila Davide zitiphunzitsa ciani pankhani ya pemphelo? (w08 3/15 14 ndime 13 CN)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal. 52:1– 53:6
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Gaŵilani kamodzi ka tumapepala twauthenga. Fotokozani za cidindo cimene cili kothela kwa kapepala kauthenga.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo ca mmene mungacitile ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila kapepala kauthenga.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Uthenga Wabwino phunzilo 3 ndime 2-3—Tsilizani mwa kukamba mau oonetsa kuti mufuna kutambitsa vidiyo ya pa jw.org yakuti, Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona?
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Zosoŵa za pampingo: (Mph. 7)
“Mulungu Ndiye Mthandizi Wanga”: (Mph. 8) Kukambilana. Pelekani mwai kwa abale ndi alongo wakuti ayankhepo pa mafunso amene alipo kuti onse apindule. (Aroma 1:12) Limbikitsani ofalitsa kuti aziseŵenzetsa Buku Lofufuzila Nkhani kuti apeze thandizo la m’Mau a Mulungu akakumana ndi mavuto.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 18 ndime 14-21, ndi kubwelelamo pa tsa. 161
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 121 ndi Pemphelo