June 6-12
MASALIMO 34-37
Nyimbo 95 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khulupilila Yehova Ndipo Cita Zabwino”: (Mph. 10)
Sal. 37:1, 2—Ikani maganizo anu pa kutumikila Yehova, m’malo moganizila anthu oipa amene aoneka ngati zinthu ziwayendela bwino (w03 12/1 9-10 ndime 3-6 CN)
Sal. 37:3-6—Khulupililani Yehova, citani zabwino, ndipo mudzadalitsidwa (w03 12/1 10-12 ndime 7-15 CN)
Sal. 37:7-11—Yembekezelani Yehova moleza mtima mpaka ataononga anthu oipa (w03 12/1 13 ndime 16- 20 CN)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 34:18—Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu a “mtima wosweka” ndi “odzimvela cisoni mumtima mwao”? (w11 6/1 19 CN)
Sal. 34:20—Kodi ulosi umenewu unakwanilitsidwa bwanji pa Yesu? (w13 12/15 21 ndime 19 CN)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Salimo 35:19–36:12
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani mavidiyo a maulaliki a citsanzo, ndipo kambilanani mfundo zake. Limbikitsani ofalitsa kukonza ulaliki wao.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa”: (Mph. 15) Kukambilana. Kuti mumvetsetse mfundo za pa kamutu kakuti “Mmene Tingacitile,” tambitsani vidiyo ya pa jw.org yakuti Ndani Analemba Baibulo? (Pitani polemba kuti MABUKU > MABUKU NDI TUMABUKU. Ndiyeno, pezani kabuku kakuti Uthenga Wabwino. Vidiyo imeneyi ipezeka pansi pankhani yakuti “Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?”)”)
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 17 ndime 1-13
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 61 ndi Pemphelo