UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa
CIFUKWA CAKE KULI KOFUNIKA:
Mavidiyo amafika anthu pamtima, cifukwa anthuwo amakopeka ndi zimene aona ndi kumva. Izi zimathandiza kuti iwo asaiŵale mfundo zimene amvela. Yehova anatipatsa citsanzo cabwino kwambili pankhani yoseŵenzetsa zinthu zooneka pophunzitsa.—Mac. 10:9-16; Chiv. 1:1.
Vidiyo yakuti Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?, Ndani Analemba Baibulo?, ndi yakuti Kodi Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona?, aonjezela mfundo za mu phunzilo 2 ndi 3 m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino. Vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?, Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji?, ndi yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu?, amalimbikitsa anthu kuphunzila Baibulo ndi Mboni, kapena kupezeka pa misonkhano ya mpingo. Mavidiyo athu ena atali, tingawagwilitsile nchito pophunzitsa ena Baibulo.—km 5/13 3.
MMENE TINGACITILE:
-
Nthawi ikaliko, citani daunilodi vidiyo imene mufuna kutambitsa mwininyumba
-
Konzani funso limodzi kapena aŵili amene adzayankhidwa m’vidiyo imeneyo
-
Onelelani vidiyo imeneyo pamodzi ndi mwininyumba
-
Kambilanani naye mfundo zazikulu
YESANI KUCITA IZI:
-
Pitani patsamba lothela la kapepala kauthenga, ndipo muonetseni cidindo cimene citsogolela ku vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?
-
Muonetseni vidiyo yakuti Kodi Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona? Ndiyeno, m’gaŵileni kabuku ka Uthenga Wabwino, ndi kufotokoza mfundo za m’phunzilo 3