UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Makolo Thandizani Ana Anu Kuti Apambane
Makolo oopa Mulungu amafunitsitsa kuti ana awo ayambe kutumikila Yehova mokhulupilika. Kuti izi zitheke, makolo afunika kukhomeleza mfundo za m’Baibo m’mitima ya ana awo kungoyambila ali akhanda. (Deut. 6:7; Miy. 22:6) Ndithudi, kucita zimenezi kumafuna kudzimana. Ndipo kudzimanako kumakhala na mapindu ambili.—3 Yoh. 4.
Makolo angaphunzile zambili kwa Yosefe na Mariya. Iwo “caka ndi caka . . . anali kukonda kupita ku Yerusalemu, ku cikondwelelo ca Pasika,” olo kuti kucita zimenezi kunali kulila mphamvu na ndalama. (Luka 2:41) Mwacionekele, Yosefe na Mariya anali kuona kuti cofunika kwambili m’banja mwawo ni kuika zinthu zauzimu patsogolo. Mofananamo, makolo masiku ano angatsogolele ana awo pa njila yoyenelela mwa kuwaphunzitsa pa mpata uliwonse umene angapeze mwa zokamba na citsanzo cawo.—Sal. 127:3-5.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI SANALEKELELE MWAYI ULIWONSE WA UTUMIKI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILA:
-
Kodi m’bale Jon na mlongo Sharon Schiller anakwanitsa bwanji kuika zinthu za Ufumu patsogolo polela ana awo?
-
N’cifukwa ciani makolo afunika kuphunzitsa na kulangiza mwana aliyense mogwilizana na mmene alili?
-
Kodi makolo angawakonzekeletse bwanji ana awo kuti asagonje ku zinthu zoyesa cikhulupililo cawo?
-
Ni zida ziti za gulu la Yehova zimene munaseŵenzetsapo pothandiza ana anu kukula mwauzimu?