June 25–July 1
LUKA 4-5
Nyimbo 37 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kanizani Ziyeso Mmene Yesu Anacitila” (10 min.)
Luka 4:1-4—Yesu sanagonje ku cilako-lako ca thupi (w13 8/1 peji 25 pala. 8)
Luka 4:5-8—Yesu sanatengeke na cilako-lako ca maso (w13 8/1 peji 25 pala. 10)
Luka 4:9-12—Yesu anakana kucita zinthu modzionetsela [Tambitsani vidiyo yopanda mau yakuti Pamwamba pa Cipupa ca Mpanda wa Kacisi.] (“Pamwamba pa Cipupa ca Mpanda wa Kacisi” nwtsty zithunzi; w13 8/1 peji 26 pala. 12)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Luka 4:17—N’ciani cionetsa kuti Yesu anali kuwadziŵa bwino Mau a Mulungu? (“mpukutu wa mneneri Yesaya” nwtsty mfundo younikila)
Luka 4:25—Kodi cilala cinatenga nthawi itali bwanji m’nthawi ya Eliya? (“zaka zitatu ndi miyezi 6” nwtsty mfundo younikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Luka 4:31-44
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kubwelelako Kaciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno, musiyileni kakhadi kongenela pa Webusaiti yathu.
Kubwelelako Kacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Sankhani mwekha lemba na kugaŵila cofalitsa cophunzitsila Baibo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) jl phunzilo 28
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Pewani Misampha Poceza ndi Anthu pa Intaneti”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Muzisamala Poceza ndi Anthu pa Intaneti.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 26
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 105 na Pemphelo