Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tsatilani Mapazi a Khristu Mosamala Kwambili

Tsatilani Mapazi a Khristu Mosamala Kwambili

Yesu anapeleka citsanzo cimene tiyenela kutengela, maka-maka ngati tikuyesedwa kapena kuzunzidwa. (1 Pet. 2:21-23) Olo kuti Yesu ananyozedwa na kuvutitsidwa, iye sanabwezele. (Maliko 15:29-32) N’ciani cinamuthandiza kupilila? Anali wofunitsitsa kucita cifunilo ca Yehova. (Yoh. 6:38) Cina, anasumika maganizo ake pa “cimwemwe cimene [Mulungu] anamuikila patsogolo pake.”—Aheb. 12:2.

Kodi timacita ciani ngati tivutitsidwa cifukwa ca cikhulupililo cathu? Akhristu oona ‘sabwezela coipa pa coipa.’ (Aroma 12:14, 17) Ngati titengela citsanzo ca Khristu ca kupilila, tidzakhala acimwemwe podziŵa kuti Mulungu akutiyanja.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:12-14.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI DZINA LA YEHOVA N’LOFUNIKA KWAMBILI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Pamene Mlongo Pötzinger * anali m’ndende ya yekha, kodi anaiseŵenzetsa bwanji nthawi mwanzelu?

  • Ni mavuto anji amene M’bale na Mlongo Pötzinger anapilila pamene anali m’ndende za cibalo?

  • N’ciani cinawathandiza kupilila?

Mukamavutika, muzitsatila mapazi a Khristu mosamala kwambili

^ par. 6 Dzinali amailembanso kuti Poetzinger.