Ali pa maceza Acikhristu ku Myanmar

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO June 2019

Makambilano Acitsanzo

Makambilano otsatizana-tsatizana okamba za zimene tingacite kuti tikakhaleko pambuyo pa masiku otsiliza.

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Nkhani ‘Yophiphilitsila’ Yokhala na Tanthauzo kwa Ife

Kodi Sara na Hagara, akazi a Abulahamu aimila ciani? Kodi pangano latsopano lingakupindulitseni bwanji?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Colinga ca Dongosolo la Mulungu

Kodi dongosolo la Mulungu n’ciani? Nanga mungacite ciani kuti mukhale ogwilizana nalo?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pangitsani Phunzilo Lanu Laumwini Kukhala Lopindulitsa

N’ciani cingakuthandizeni kuti muzikhala na phunzilo laumwini lopindulitsa?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Valani Zida Zonse Zankhondo Zocokela kwa Mulungu”

Akhristu ni asilikali. Chulani dzina la cida ciliconse ca nkhondo yanu yauzimu, na kufotokoza zimene citanthauza.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Yehova Aiona Bwanji Nkhaniyi?

Kodi mungatani kuti mupitilize kuzindikila cifunilo ca Yehova na kucita mogwilizana naco?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Musamade Nkhawa ndi Kanthu Kalikonse”

Timada nkhawa na zinthu zambili m’masiku otsiliza ano. N’ciani cingakuthandizeni kucepetsa nkhawa?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Sankhani Zosangalatsa Mwanzelu

Kodi nthawi yanu yopumula mungaiseŵenzetse bwanji kuti mukondweletse Mulungu?