UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pangitsani Phunzilo Lanu Laumwini Kukhala Lopindulitsa
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Phunzilo laumwini limatithandiza ‘kudziŵa bwino m’lifupi, m’litali, kukwela, na kuzama’ kwa coonadi. (Aef. 3:18) Limatithandizanso kuti tikhale opanda cifukwa cotineneza naco, osalakwa m’dziko lino loipa komanso “kugwila mwamphamvu mawu amoyo.” (Afil. 2:15, 16) Pa phunzilo laumwini timasankha nkhani zimene tifuna kuphunzila. Tingacite ciani kuti tizipindula mofikapo pamene tiŵelenga na kuphunzila Baibo?
MMENE TINGACITILE:
-
Congani mavesi na kulemba mfundo m’Baibo yanu yopulinta kapena ya pa cipangizo
-
Poŵelenga Mawu a Mulungu, dzifunseni mafunso aya: ‘N’ndani? N’ciani? Liti? N’kuti? Cifukwa ciani? Motani?’
-
Pezani mfundo. Seŵenzetsani zida zofufuzila zimene zilipo. Mungafufuze mwa kuseŵenzetsa mutu wa nkhani kapena lemba
-
Muzisinkha-sinkha zimene mwaŵelenga kuti muone mmene mfundozo zingakuthandizileni mu umoyo wanu
-
Seŵenzetsani zimene mwaphunzila mu umoyo wanu.—Luka 6:47, 48
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI PITILIZANI “KUGWILA MWAMPHAMVU” MWA KUCITA PHUNZILO LAUMWINI LOPINDULITSA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
Kodi ena amacita bwanji phunzilo laumwini?
-
N’cifukwa ciani tifunika kupemphela tisanayambe phunzilo laumwini?
-
N’ciani cingatithandize kuimvetsa bwino Baibo?
-
Ni zizindikilo zanji zimene tingaike m’Baibo imene timaseŵenzetsa?
-
N’cifukwa ciani kusinkha-sinkha n’kofunika poŵelenga Mawu a Mulungu?
-
Kodi tiyenela kucita nazo ciani zimene timaŵelenga?