Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Sankhani Zosangalatsa Mwanzelu

Sankhani Zosangalatsa Mwanzelu

N’cifukwa ciani tifunika kusankha zosangalatsa mwanzelu? Cifukwa pamene tisankha filimu yotamba, nyimbo yomvetsela, webusaiti yoti tiloŵepo, buku loti tiŵelenge, kapena gemu ya pavidiyo kuti tichaye, timakhala tikusankha zinthu zoti zikhale m’maganizo mwathu. Conco, zimene timasankha zimakhudza khalidwe lathu. N’zomvetsa cisoni kuti, zosangalatsa zambili masiku ano n’zodzala na zinthu zimene Yehova amadana nazo. (Sal. 11:5; Agal. 5:19-21) N’cifukwa cake Baibo imatilangiza kuti sitifunika kuleka kuganizila zinthu zolemekeza Yehova.—Afil. 4:8.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KODI NIYENELA KUSANKHA ZOSANGALATSA ZABWANJI? PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi maseŵela omenyana a ku Roma wakale afanana bwanji na zosangalatsa zina zamakono?

  • Kodi abale na alongo mu mpingo angathandize bwanji acicepele kusankha zosangalatsa mwanzelu?

  • Kodi lemba la Aroma 12:9 lingatithandize bwanji posankha zosangalatsa?

  • Ni zosangalatsa zotani zabwino zimene zimacitika m’dela lanu?