June 3-9
AGALATIYA 4-6
Nyimbo 16 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Nkhani ‘Yophiphilitsila’ Yokhala na Tanthauzo kwa Ife”: (10 min.)
Agal. 4:24, 25—Hagara anaimila Aisiraeli amene anali m’pangano la Cilamulo (it-1 1018 ¶2)
Agal. 4:26, 27—Sara anaimila ‘Yerusalemu wakumiyamba,’ amene ni gawo lakumwamba la gulu la Yehova (w14 10/15 10 ¶11)
Agal. 4:28-31—Madalitso kwa anthu omvela adzabwela kupitila mwa “ana” a Yerusalemu wakumiyamba
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Agal. 4:6—Kodi liwu la Ciheberi kapena la Ciaramu lakuti abba litanthauza ciani? (w09 4/1 13)
Agal. 6:17—Kodi mtumwi Paulo ayenela kuti anakhala na “zipsela za cizindikilo ca kapolo wa Yesu” m’njila ziti? (w10 11/1 15)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Agal. 4:1-20 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kumveketsa Bwino Cifukwa Coŵelengela Lemba. Ndiyeno, kambilanani phunzilo 6 m’bulosha ya Kuphunzitsa.
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w12 3/15 30-31—Mutu: N’cifukwa Ciani Mkhristu Afunika Kupewelatu Zamalisece? (th phunzilo 13)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (8 min.)
Zimene Gulu Likukwanilitsa: (7 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa ya June.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 69
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 40 na Pemphelo