Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AGALATIYA 4-6

Nkhani ‘Yophiphilitsila’ Yokhala na Tanthauzo kwa Ife

Nkhani ‘Yophiphilitsila’ Yokhala na Tanthauzo kwa Ife

4:24-31

Mtumwi Paulo anasimba nkhani ‘yophiphilitsila,’ pofuna kuonetsa kuti pangano latsopano n’labwino kuposa pangano la Cilamulo. Khristu pamodzi na olamulila anzake adzatiyang’anila mwacikondi. Ndipo tonse tidzamasulidwa ku ucimo, kupanda ungwilo, mavuto, komanso imfa.—Yes. 25:8, 9.

 

HAGARA—KAPOLO WAMKAZI

Isiraeli wakuthupi amene anali m’pangano la Cilamulo. Likulu lake linali Yerusalemu

SARA—MFULU

Yerusalemu wakumiyamba, amene ni gawo lakumwamba la gulu la Mulungu

“ANA” A HAGARA

Ayuda (amene analonjeza kuti azitsatila pangano la Cilamulo) anazunza Yesu, ndipo anamukana

“ANA” A SARA

Khristu na Akhristu odzozedwa okwana 144,000

UKAPOLO KU PANGANO LA CILAMULO

Cilamuloci cinali kukumbutsa Aisiraeli kuti anali akapolo a ucimo

PANGANO LATSOPANO LIMATIPATSA UFULU

Kukhulupilila nsembe ya Khristu kunabweletsa ufulu wotimasula ku ukapolo wa Cilamulo