June 22-28
EKSODO 1-3
Nyimbo 7 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Eksodo.]
Eks. 3:13—Mose anali kufuna kudziŵa zambili za uyo amene dzina lake ni Yehova (w13 3/15 25 ¶4)
Eks. 3:14—Yehova amakhala ciliconse cofunikila kuti akwanilitse colinga cake (kr 43, bokosi)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 2:10—N’cifukwa ciani n’zoveka kukhulupilila kuti mwana wa mkazi wa Farao anatenga Mose kukhala mwana wake? (g04 4/8 6 ¶5)
Eks. 3:1—Kodi Yetero anali wansembe wotani? (w04 3/15 24 ¶4)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 2:11-25 (th phunzilo 11)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, kopani cidwi cake. (th phunzilo 16)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo, ndiyeno gaŵilani magazini ya posacedwa yogwilizana na nkhani imene mwakambilana na mwininyumba. (th phunzilo 12)
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w02 6/15 11 ¶1-4 —Cinthu Coposa Cuma ca Aiguputo. (th phunzilo 13)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khala Bwenzi la Yehova—Dzina la Yehova: (6 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno, ngati n’zotheka, pemphani ana amene munasankhilatu kuti abwele ku pulatifomu, kenako afunseni kuti: Kodi dzina la Yehova limatanthauzanji? Kodi Yehova analenga zinthu zotani? Nanga Yehova angakuthandizeni bwanji?
Dzina la Mulungu Likwezedwa ku Scandinavia: (9 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela: N’cifukwa ciani ni anthu ocepa cabe amene anali kudziŵa dzina la Mulungu cisanafike caka ca 1500? Kodi dzina lakuti Yehova linayamba bwanji kuseŵenzetsedwa ku Scandinavia? N’cifukwa ciani mumayamikila Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 120
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 104 na Pemphelo