Akucita Cikumbutso ca Imfa ya Kristu ku Germany

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO March 2016

Maulaliki Acitsanzo

Maulaliki acitsanzo ogaŵila Nsanja ya Mlonda ndi kapepala koitanila anthu ku Cikumbutso ka 2016. Seŵenzetsani maulaliki acitsanzo amenewa kuti mukonze ulaliki wanu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Esitere Anaimila Yehova ndi Anthu Ake

Molimba mtima iye anaika moyo wake pangozi, ndipo anathandiza Moredekai kulemba lamulo lakuti Ayuda asaphedwe. (Esitere 6-10)

KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Konzani Ulaliki Wanu Wogaŵila Magazini

Gwilitsilani nchito maulaliki acitsanzo kuti mukonze ulaliki wanu wogaŵila Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani!

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Landilani Alendo

Kodi tingathandize bwanji alendo ndi ozilala kudzimva kuti ndi olandilidwa pa Cikumbutso?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa

Iye anaonetsa kuti Yehova ndi wofunika kwambili paumoyo wake. (Yobu 1-5)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Munthu Wokhulupilika Yobu Afotokoza Mavuto Ake

Mavuto aakulu amene Yobu anakumana nao anakhudza mmene iye anali kuonela zinthu, koma anapitiliza kukonda Yehova Mulungu. (Yobu 6-10)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Yobu Anali ndi Cikhulupililo Cakuti Akufa Adzauka

Anali kudziŵa kuti Mulungu adzamuukitsa, mofanana ndi kuphukilanso kwa citsa couma ca mtengo. (Job 11-15)

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Ciukililo Cidzatheka Kupitila mu Nsembe ya Dipo

Mphatso ya Yehova ya dipo idzacititsa kuti ciukililo ca mtsogolo cikakhale cotheka. M’malo moika malilo, tizikalandila anthu amene adzaukitsidwa.