Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Maulaliki Acitsanzo

Maulaliki Acitsanzo

NSANJA YA MLONDA

Funso: Kodi mau odziŵika bwino awa mumawamvetsetsa?

Lemba: Yoh. 3:16

Kugaŵila Cofalitsa: Nsanja ya Mlonda iyi, ifotokoza mapindu amene mungapeza cifukwa cakuti Yesu anavutika ndi kutifela.

NSANJA YA MLONDA (tsamba lothela)

Funso: Onani funso ili ndi mayankho amene anthu ambili apeleka. [Ŵelengani funso loyamba ndi mayankho ake.] Kodi inu mungayankhe bwanji?

Lemba: Mat. 4:1-4

Kugaŵila Cofalitsa: Popeza Mdyelekezi anakamba ndi Yesu ndi kumuyesa, ndiye kuti Mdyelekezi alikodi osati kuti ndi maganizo oipa cabe. Kodi Baibulo limakamba ciani za Mdyelekezi? Magazini iyi ikufotokoza zambili.

KAPEPALA KOITANILA ANTHU KU CIKUMBUTSO

Kugaŵila Kapepala: Tikupatsa anthu tumapepala towaitanila ku mwambo wofunika kwambili. [Patsani mwininyumba kapepala.] Pa March 23, anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi adzasonkhana kuti akumbukile imfa ya Yesu Kristu, ndi kumvetsela ku nkhani ya m’Baibulo yaulele imene idzafotokoza mapindu amene tidzapeza cifukwa ca imfa yake. Pa kapepala aka alembapo malo ndi nthawi kumene kudzacitikila mwambo umenewu kuno kwathu. Conde mukabwele.”

LEMBANI ULALIKI WANU

Onani maulaliki acitsanzo amene asonyezedwa kale kuti akuthandizeni kulemba ulaliki wanu.