March 14- 20
YOBU 1-5
Nyimbo 89 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa”: (Mph. 10)
[Onetsani vidiyo yofotokoza Mfundo Zokhudza Buku la Yobu. Ngati n’zosatheka kuonelela vidiyo, yambani kukamba nkhani yakuti “Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa.”]
Yobu 1:8-11—Satana anakaikila kukhulupilika kwa Yobu (w11–CN 5/15 17 ndime 6-8; w09–CN 4/15 3 ndime 3-4)
Yobu 2:2-5—Satana anakaikila zakuti anthu onse angakhale okhulupilika (w09–CN 4/15 4 ndime 6)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8)
Yobu 1:6; 2:1—Ndani ankaloledwa kuonekela kwa Yehova? (w06–CN 3/15 13 ndime 6)
Yobu 4:7, 18, 19—Ndi maganizo olakwika ati amene Elifazi anauza Yobu? (w14–CIN 3/1 12 ndime 3; w05–CN 9/15 26 ndime 4-5; w95–CN 2/15 27 ndime 5-6)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwandiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Yobu 4:1-21 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya 2016 Na.2 pacikuto. Yalani maziko a ulendo wobwelelako. (Mph. 2 kapena zocepelapo)
Ulendo wobwelelako: Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya 2016 Na.2 pacikuto. Yalani maziko a ulendo wina wobwelelako. (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Phunzilo la Baibulo: fg phunzilo 2 ndime 2-3 (Mph. 6 kapena zocepelapo)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
Pewani Kusonkhezeledwa ndi Anzanu: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyo ya pa jw.org yakuti Stand Up to Peer Pressure! (Pitani polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACINYAMATA. Ngati n’zosatheka kambani mfundo za m’buku la Zimene Acinyamata Amafunsa Voliyamu 2 mutu 15 mas. 129-130.) Mukatsiliza, funsani mafunso otsatilawa: Kodi ana amakumana ndi mayeselo otani kusukulu? Kodi angagwilitsile nchito bwanji mfundo ya pa Ekisodo 23:2? Ndi njila zinai ziti zimene zingawathandize kulimbana ndi ziyeso ndi kukhalabe okhulupilika? Pemphani acinyamata kuti afotokoze zocitika zosangalatsa.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 11 ndime 1-11 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zimene Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 133 ndi Pemphelo