Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Ciukililo Cidzatheka Kupitila mu Nsembe ya Dipo

Ciukililo Cidzatheka Kupitila mu Nsembe ya Dipo

Cikumbutso cimatipatsa mwai woganizila madalitso a mtsogolo amene adzatheka cifukwa ca nsembe ya dipo, monga ciukililo. Yehova sanafune kuti anthu azifa. N’cifukwa cake anthu amavutika ndi cisoni munthu amene amamukonda akamwalila. (1 Akor. 15:26) Yesu anamva cisoni ataona kuti ophunzila ake akulila cifukwa ca imfa ya Lazaro. (Yoh. 11:33-35) Popeza kuti Yesu ndi cifanizilo ca Atate wake, tingakhale otsimikiza kuti nayenso Yehova cimamuŵaŵa akaona kuti tikuvutika ndi cisoni kaamba ka imfa ya munthu amene timakonda. (Yoh. 14:7) Yehova amalakalaka nthawi imene adzaukitsa atumiki ake okhulupilika. Nafenso timalakalaka zimenezo.—Yobu 14:14, 15.

Popeza kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo, m’pomveka kukhulupilila kuti ciukililo cidzacitika mwadongosolo. (1 Akor. 14:33, 40) M’malo moika malilo, tizikalandila anthu amene adzaukitsidwa. Kodi mumaganizila mozama pa ciukililo, makamaka pa nthawi imene muli ndi cisoni? (2 Akor. 4:17, 18) Kodi mumayamikila Yehova kaamba kotipatsa nsembe ya dipo, ndi kutifotokozela m’Malemba kuti akufa adzakhalanso ndi moyo?—Akol. 3:15.

  • Ndi anzanu komanso acibale anu ati amene mufunitsitsa kudzawaonanso?

  • Ndi anthu ati ochulidwa m’Baibulo amene mufunitsitsa kudzaceza nao?