Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 11-15

Yobu Anali ndi Cikhulupililo Cakuti Akufa Adzauka

Yobu Anali ndi Cikhulupililo Cakuti Akufa Adzauka

Yobu anaonetsa kuti anali ndi cikhulupililo cakuti Mulungu adzamuukitsa

14:7-9, 13-15

  • Yobu anaonetsa cikhulupililo cake cakuti Mulungu adzaukitsa akufa pamene anayelekezela ciyembekezoco ndi mtengo, mwina wa maolivi

  • Mtengo wa maolivi akaudula umaphukanso cifukwa cakuti mizu yake imapita pansi kwambili ndiponso imayala malo aakulu. Ngati mizu yake ikali bwino, mtengowu sulephela kuphuka

  • Mvula ikagwa pambuyo pa cilala coopsa, mizu ya citsa couma ca mtengo wa maolivi imaphuka n’kukhala ndi “nthambi ngati mtengo watsopano”