March 7- 13
ESITERE 6-10
Nyimbo 131 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Esitere Anaimila Yehova ndi Anthu Ake”: (Mph. 10)
Esitere 8:3, 4—Ngakhale kuti Esitere anali wotetezeka, iye anaika moyo wake pangozi cifukwa ca anthu ena (ia 143 ndime 24-25)
Esitere 8:5—Esitere anacita zinthu mwanzelu ndi Ahasiwero (w06–CN 3/1 11 ndime 8)
Esitere 8:17—Anthu ambili analoŵa Ciyuda (w06–CN 3/1 11 ndime 3)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8)
Esitere 8:1, 2—Kodi ulosi umene Yakobo anakamba ali pafupi kufa wakuti Benjamini adzagaŵa zimene wafunkha madzulo, unakwanilitsidwa bwanji? (ia 142 pa kabokosi)
Esitere 9:10, 15, 16—Ngakhale kuti lamulo linalola kulanda zofunkha, n’cifukwa ciani Ayuda sanacite zimenezo? (w06–CN 3/1 11 ndime 4)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwandiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Esitere 8:1-9 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani mavidiyo a maulaliki acitsanzo ndi kukambilana mfundo zake. Ngati n’zosatheka kuonelela mavidiyo, ofalitsa aluso acite zitsanzo. Kenako, kambilanani nkhani yakuti “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Konzani Ulaliki Wanu Wogaŵila Magazini.”
UMOYO WATHU WACIKRISTU
“Landilani Alendo”: (Mph. 15) Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zosangalatsa zimene anapeza, cifukwa colandila alendo panthawi ya Cikumbutso caka catha. Citani citsanzo ca cocitika cimodzi cosangalatsa.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 10 ndime 12-21, ndi kubwelelamo pa tsa. 91 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 69 ndi Pemphelo