Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Konzani Ulaliki Wanu Wogaŵila Magazini

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Konzani Ulaliki Wanu Wogaŵila Magazini

CIFUKWA CAKE KULI KOFUNIKA: Ngakhale kuti maulaliki acitsanzo amene ali m’kabuku ka msonkhano amapeleka malangizo othandiza, amenewa ndi maautilaini cabe. Mufunika kukamba m’mau anuanu. Mungasankhe njila ina ya ulaliki kapena nkhani imene ingakhale yogwila mtima m’dela lanu. Mukaŵelenga magazini, kukambilana maulaliki acitsanzo, ndi kuonelela mavidiyo, mungaseŵenzetse mfundo zotsatilazi kuti mukonze ulaliki wanu.

MMENE MUNGACITILE:

Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndifuna kuseŵenzetsa ulaliki wacitsanzo?’

INDE

  • Konzekelani mau anu oyamba. Mukapeleka moni, fotokozani mwacidule cimene mwabwelela. (Mwacitsanzo: “Ndabwela kuti  . . . ”)

  • Ganizilani mmene mudzafunsila funso, pamene mudzaŵelenga lemba, ndi kugaŵila cofalitsa. (Mwacitsanzo: Kuti muŵelenge lemba, mungakambe kuti: “Yankho la funso limeneli tilipeza pa lemba ili.”)

IYAI

  • Sankhani nkhani kucokela m’magazini imene ingakope cidwi ca anthu a m’gawo lanu

  • Sankhani funso limene lingacititse kuti muyambe kukambilana, koma musafunse funso lopanikiza mwininyumba. (Mwacitsanzo: Onani mafunso amene ali pa tsamba 2.)

  • Sankhani lemba lakuti muŵelenge. (Ngati mukugaŵila Galamukani! mungasankhe kuŵelenga lemba kapena ai, cifukwa magazini imeneyi amalembela anthu amene sadziŵa zambili za Baibulo, ndipo amakaikila za cipembedzo.)

  • Konzani tumau twacidule tofotokoza mapindu amene mwininyumba angapeze akaŵelenga nkhaniyo

KAYA MUSEWENZETSA ULALIKI WACITSANZO KAPENA AI

  • Konzekelani funso limene mudzayankha pa ulendo wobwelelako

  • Lembani manotsi kuti mukakumbukile zimene mukakambe