Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Landilani Alendo

Landilani Alendo

Pa March 23, anthu oposa 12 miliyoni adzabwela ku Cikumbutso monga alendo athu. Iwo adzamvetsela kwa mkambi amene adzafotokoza mphatso ya dipo imene Yehova watipatsa, ndi madalitso ena a mtsogolo amene anthu adzalandila. (Yes. 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23; Yoh. 3:16) Komabe, si mkambi cabe amene adzacitila umboni pa cocitika capadela cimeneci. Tonsefe tidzakhala ndi mwai wolandila alendo. (Aroma 15:7) Onani zimene tifunika kucita.

  • M’malo mongokhala pampando ndi kuyembekezela pulogalamu kuti iyambe, landilani alendo ndiponso anthu ofooka mwa kumwetulila ndi kuwapatsa moni mwaubwenzi

  • Mukamalandila mabwenzi amene munaitanila, mulandilenso ena amene abwela cifukwa cakuti analandila kapepala ka ciitano. Pemphani atsopano kuti mukhale nao pamodzi, ndipo ŵelengani nao pamodzi Baibulo ndi kuona nao m’buku lanu nyimbo

  • Nkhani ikatha, khalani wofunitsitsa kuyankha mafunso amene angakhale nao. Ngati mpingo wanu uyenela kucoka pa Nyumba ya Ufumu mwamsanga kuti ena asonkhanilanepo, pangani makonzedwe akuti mukaonane ndi munthuyo mwamsanga. Ngati simudziŵa kumene akhala, mungamuuze kuti: “Ndingakonde kumva mmene mwaonela msonkhanowu. Kodi ndingakupezeni bwanji?”