Aitanila anthu ku Mgonelo wa Ambuye ku Albania

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO March 2017

Maulaliki a Citsanzo

Maulaliki a citsanzo oseŵenzetsa pogaŵila Nsanja ya Mlonda ndi pophunzitsa mfundo ya coonadi yokhudza Ufumu wa Mulungu. Seŵenzetsani maulaliki a citsanzo pokonza ulaliki wanu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

“Ine Ndili ndi Iwe Kuti Ndikulanditse”

Pamene Yehova Mulungu anasankha Yeremiya kukhala mneneli, Yeremiya anadziona kuti niwosayenelela udindowo. Kodi Yehova anam’tsimikizila ciani?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Analeka Kucita Cifunilo ca Mulungu

Aisiraeli anaganiza kuti nsembe zamwambo zingalungamitse macimo awo. Molimba mtima, Yeremiya anavumbula macimo a Aisiraeli na cinyengo cawo.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kuseŵenzetsa Kabuku Kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?

Seŵenzetsani kabukuka kuti muthandize ophunzila Baibo anu kudziŵa bwino Mboni za Yehova, ndi kuwathandiza kudziŵa bwino nchito yathu na gulu lathu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Anthu Angapambane Kokha Ngati Atsogozedwa na Yehova

Mu nthawi ya Aisiraeli, anthu amene anali kutsatila citsogozo ca Yehova Mulungu anali kukhala mwa mtendele, mwa cimwemwe, ndipo zinthu zinali kuwayendela bwino.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kuseŵenzetsa Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu?

Seŵenzetsani mapikica na malemba kuti muphunzitse mfundo zoyambilila za coonadi kwa anthu amene sakwanitsa kuŵelenga bwino-bwino.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Aisiraeli Anaiŵala Yehova

Kodi Yehova anali kuonetsa ciani pamene anauza Yeremiya kuyenda makilomita pafupi-fupi 500 kupita ku mtsinje wa Firate kuti akabitse lamba wansalu?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Thandizani a m’Banja Lanu Kukumbukila Yehova

Kucita Kulambila kwa Pabanja kwatanthauzo nthawi zonse kungathandize banja lanu kukumbukila Yehova. Mungathetse bwanji zopinga zofala zimene zingalepheletse kulambila kwa pabanja?