March 13-19
YEREMIYA 5-7
Nyimbo 66 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Analeka Kucita Cifunilo ca Mulungu”: (10 min.)
Yer. 6:13-15—Yeremiya anavumbula macimo a mtundu wa Aisiraeli (w88 4/1 peji 11-12 mapala. 7-8)
Yer. 7:1-7—Yehova anayesa kuwathandiza kuti alape (w88 4/1 peji 12 mapala. 9-10)
Yer. 7:8-15—Aisiraeli anali kuona monga Yehova sadzacitapo kanthu (jr peji 21 pala. 12)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 6:16—Kodi Yehova analimbikitsa anthu ake kucita ciani? (w05 11/1 peji 23 pala. 11)
Yer. 6:22, 23—N’cifukwa ciani tingati anthu anali ‘kudzabwela kucokela kudziko la kumpoto’? (w88 4/1 peji 13 pala. 15)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 5:26–6:5
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) T-36—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) T-36—Kambilanani kamutu kakuti “Ganizilani Funso Ili.” Itanilani munthuyo ku Cikumbutso.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) jl phunzilo 1—Itanilani munthuyo ku Cikumbutso.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kuseŵenzetsa Kabuku Kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?”: (15 min.) Yambani mwa kufotokoza nkhaniyi kwa 5 mineti. Ndiyeno tambitsani na kukambilana vidiyo yoonetsa mmene tingaseŵenzetsele kabukuka pa phunzilo 8. Limbikitsani onse amene amatsogoza maphunzilo a Baibo kuti aziseŵenzetsa kakubuka wiki iliyonse.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 9 mapala. 16-21, bokosi papeji 94, na bokosi lobwelelamo papeji 95
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 10 na Pemphelo