Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kuseŵenzetsa Kabuku Kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?

Kuseŵenzetsa Kabuku Kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?

Kabuku kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? kanakonzedwa kuti tizikambilana mfundo zake ndi ophunzila Baibo athu, kuciyambi kapena kumapeto kwa phunzililo lililonse. * Maphunzilo 1 mpaka 4 amathandiza ophunzila athu kuzidziŵa bwino Mboni za Yehova. Maphunzilo 5 mpaka 14 amawathandiza kudziŵa bwino nchito yathu. Ndipo maphunzilo 15 mpaka 28 amawathandiza kudziŵa zimene gulu lathu limacita. Zimakhala bwino kuphunzila kabukuka motsatila dongosolo la maphunzilo ake, kupatula ngati pakhala kufunikila kokambilana naye phunzilo linalake. Phunzilo iliyonse ili papeji imodzi cabe. Ndipo ophunzila ambili mungakambilane nawo kwa mamineti 5 kapena 10 cabe.

  • Muonetseni funso imene ni mutu wa phunzilolo

  • Ŵelengani naye phunzilolo, kaya lonse kapena m’zigawo-zigawo

  • Kambilanani zimene mwaŵelenga. Funsani mafunso ali munsi mwa peji, na kukambilana mapikica ake. Ŵelengani na kukambilana malemba osagwila mau oyenelela. Fotokozani kuti tumitu twakuda kwambili tuyankha funso la mutu wa phunzilo

  • Ngati muli kabokosi kakuti “Dziŵani Zambili,” ŵelengani naye ndi kum’limbikitsa kucita zimene zalembedwazo

^ par. 3 Kabuku kali pa intaneti ndiye kokonzedwanso.