March 20-26
YEREMIYA 8-11
Nyimbo 117 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Anthu Angapambane Kokha Ngati Atsogozedwa na Yehova”: (10 min.)
Yer. 10:2-5, 14, 15—Milungu ya amitundu ni milungu yonama (it-1 555)
Yer. 10:6, 7, 10-13—Mosiyana na milungu ya amitundu, Yehova yekha ndiye Mulungu woona (w04 10/1 peji 11 pala. 10)
Yer. 10:21-23—Anthu sangapambane popanda citsogozo ca Yehova (w15 9/1 peji 15 pala. 1)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 9:24—Kodi kudzitama ndi kunyada koyenela n’kotani? (w13 1/15 peji 20 pala. 16)
Yer. 11:10—N’cifukwa ciani Yeremiya popeleka uthenga wa ciweluzo anaphatikizapo ufumu wa kumpoto wa mafuko 10 ngakhale kuti Samariya anali atawonongedwa kale mu 740 B.C.E.? (w07 3/15 peji 9 pala. 2)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 11: 6-16
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) Ciitano ca ku Cikumbutso na nkhani ya pacikuto ca wp17.2—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Ciitano ca ku Cikumbutso na nkhani ya pacikuto ca wp17.2—Yalani maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) ld mapeji 4-5 (Mwininkhani angasankhe mapikica amene angakambilane.)—Itanilani munthuyo ku Cikumbutso.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kuseŵenzetsa Kabuku ka, Mvetselani kwa Mulungu?”: (15 min.) Yambani mwa kufotokoza mfundo za nkhaniyo kwa 5 mineti. Ndiyeno tambitsani na kukambilana vidiyo yoonetsa phunzilo la Baibo la pamapeji 8 na 9 m’kabukuka. Wophunzila aseŵenzetsa Mvetselani kwa Mulungu, pamene mphunzitsi wake aseŵenzetsa Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Limbikitsani omvela kuti azitsatila m’kabuku kawo ka Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr mapeji 98-99, nkhani 10 mapala. 1-7
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 35 na Pemphelo