Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kuseŵenzetsa Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu?

Kuseŵenzetsa Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu?

Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu anakakonza kuti tiziphunzitsila anthu mfundo zoyambilila za m’Baibo. Mapikica ake amathandiza kwambili anthu amene sakwanitsa kuŵelenga bwino-bwino. Phunzilo iliyonse ya pamapeji aŵili ili na mapikica okhala na tumivi tolongoza makambilano kucoka pa pikica ina kupita pa yotsatila.

Kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Kwamuyaya kali na mapikica amene alinso mu Mvetselani kwa Mulungu, koma kali na mau oculukilapo. Ophunzila amene amakwanitsako kuŵelenga bwino angaseŵenzetse kameneka. Nthawi zambili ofalitsa amakonda kukaseŵenzetsa monga buku la mphunzitsi, pamene wophunzila wawo aseŵenzetsa ka Mvetselani kwa Mulungu. Mapeji ambili ali na kabokosi ka mfundo zowonjezela, ndipo mungakambilane mfundozo malinga ndi wophunzila wanu.

Mungagaŵile tumabuku tumenetu panthawi iliyonse, ngakhale kuti si cogaŵila ca mwezi umenewo. Potsogoza phunzilo la Baibo, seŵenzetsani mapikica kuti mufotokoze nkhani za m’Baibo. Funsani mafunso kuti muloŵetsemo wophunzila ndi kutsimikizila kuti wamvetsetsa. Ŵelengani ndi kukambilana malemba ali pansi pa peji iliyonse. Mukakatsiliza kuphunzila kabukuka, kayambeni naye buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse kuti mukam’thandize kupita patsogolo ndi kukabatizika.