Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Thandizani a m’Banja Lanu Kukumbukila Yehova

Thandizani a m’Banja Lanu Kukumbukila Yehova

Yeremiya anapatsidwa nchito yocenjeza Ayuda za ciwonongeko cimene cinali kubwela pa iwo cifukwa anali ataiŵala Mulungu wawo, Yehova. (Yer. 13:25) Cinacitika n’ciani kuti umoyo wakuuzimu wa mtunduwu ufike poipa conco? Mabanja aciisiraeli sanalinso auzimu. N’zoonekelatu kuti mitu ya mabanja siinali kutsatila malangizo a Yehova a pa Deuteronomo 6:5-7.

Mabanja olimba kuuzimu amapangitsa mipingo kukhala yolimba. Mitu ya mabanja ingathandize mabanja awo kukumbukila Yehova mwa kumacititsa Kulambila kwa Pabanja kwa phindu nthawi zonse. (Sal. 22:27) Pambuyo potamba vidiyo yakuti Mau Awa . . . Azikhala Pamtima Pako”—Kufunsa Mafunso Mabanja, yankhani mafunso aya:

  • N’ciani cathandiza mabanja ena kuthetsa zopinga zofala zimene zimalepheletsa kulambila kwa pabanja?

  • Kodi pali mapindu anji ngati tikhala na Kulambila kwa Pabanja kokhazikika?

  • Pa nkhani ya kulambila kwa pabanja, n’zovuta ziti zimene ine pacanga nimakhala nazo? Nanga nakonzekela kuzithetsa bwanji?