UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO March 2018
Makambilano Acitsanzo
Makambilano ozikidwa pa kampeni yoitanila anthu ku Cikumbutso na mafunso akuti: N’cifukwa ciani Yesu anafa? Kodi dipo limatheketsa ciani?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenela Kukhala Mtumiki Wanu”
Pamene ticita mautumiki osiyana-siyana, kodi colinga cathu n’cakuti tichuke na kutamandidwa? Nthawi zambili mtumiki wodzicepetsa amacita nchito zimene sizionekela kwa anthu ena koma kwa Yehova Mulungu cabe.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Muzitsatila Malamulo Aŵili Aakulu a m’Cilamulo
Kodi Yesu anakamba kuti malamulo aŵili aakulu a m’Cilamulo opezeka m’Baibo ni ati? Tingaonetse bwanji kuti timamvela malamulo amenewa?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tingacite Ciani Kuti Tikulitse Cikondi Cathu kwa Mulungu na kwa Mnansi Wathu
Tifunika kukonda Mulungu na mnansi wathu. Njila imodzi imene ingatithandize kukulitsa khalidwe la cikondi ni mwa kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Khalanibe Ogalamuka m’Masiku Otsiliza Ano
Masiku ano, kufuna-funa zinthu za kuthupi kwacititsa anthu ambili kulephela kucita zinthu zauzimu. Kodi Akhristu ogalamuka mwauzimu amasiyana bwanji ndi anthu a ku dziko?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tili ku Mapeto a Dongosolo Lino la Zinthu
Kodi mau a Yesu aonetsa bwanji kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto? Funso ili pamodzi na ena ayankhiwa m’vidiyo yakuti Tili ku Mapeto a Dongosolo Lino la Zinthu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khalanibe Maso”
M’fanizo la anamwali 10, kodi mkwati, anamwali ocenjela, ndi anamwali opusa aimila ndani? Nanga kodi fanizo limeneli likukhudzani bwanji?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuthandiza Maphunzilo Athu a Baibo Kukonzekela
Tikangokhazikitsa phunzilo, tiziwathandiza ophunzila athu kukhala na cizoloŵezi cokonzekela phunzilo. Tingacite bwanji zimenezi?