Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makambilano Acitsanzo

Makambilano Acitsanzo

●○○ ULENDO WOYAMBA

Kampeni Yoitanila Anthu ku Cikumbutso (March 3-31): Tikuitanilani ku cocitika cofunika kwambili. Kapepa kanu ka ciitanilo ni aka. Pa ciŵelu, March 31, mamiliyoni a anthu pa dziko lonse adzasonkhana kuti acite mwambo wokumbukila imfa ya Yesu Khristu. Kapepa ka ciitanilo aka kaonetsa nthawi na malo kumene msonkhano uyu udzacitikile m’dela lathu lino. Tikuitanilaninso ku nkhani imene idzakambiwa wiki ya cikumbutso isanafike. Mutu wake ni wakuti, “Kodi Yesu Khristu Ndani Maka-maka?”

Funso la Ulalo Ngati Waonetsa Cidwi: N’cifukwa ciani Yesu anafa?

○●○ KUBWELELAKO KOYAMBA:

Funso: N’cifukwa ciani Yesu anafa?

Lemba: Mat. 20:28

Ulalo: Kodi dipo limatheketsa ciani?

○○● KUBWELELAKO KACIŴILI

Funso: Kodi dipo limatheketsa ciani?

Lemba: Aroma 6:23

Ulalo: Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila dipo?