Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tingacite Ciani Kuti Tikulitse Cikondi Cathu kwa Mulungu na kwa Mnansi Wathu

Tingacite Ciani Kuti Tikulitse Cikondi Cathu kwa Mulungu na kwa Mnansi Wathu

Ngakhale kuti Akhristu sali pansi pa Cilamulo ca Mose, ico cinali na malamulo aŵili aakulu oonetsa zimene Mulungu amafuna kwa ise—kukonda Mulungu, na kukonda mnansi wako. (Mat. 22:37-39) Cikondi caconco sitibadwa naco. Tifunika kucitapo kanthu kuti tikhale naco. Motani? Njila imodzi ni kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku. Tikaganizila makhalidwe osiyana-siyana a Mulungu, amene timaŵelenga m’Baibo, timaona “ubwino wa Yehova.” (Sal. 27:4) Tikacita conco, cikondi cathu pa iye cimakula ndipo timayamba kuganiza mofanana ndi iye. Izi zimatilimbikitsa kusunga malamulo a Mulungu, amene amaphatikizapo lamulo la kuonetsa ena cikondi codzimana. (Yoh. 13:34, 35; 1 Yoh. 5:3) Nazi njila zitatu zimene zingathandize kuti kuŵelenga Baibo kwathu kuzikhala kokondweletsa:

  • M’maganizo mwathu, tiziyesa kuona zinthu, kumva, na kununkhiza. Muziyelekeza kuti munaliko pa nthawiyo. Kodi anthu amene akuchulidwawo anali kumvela bwanji?

  • Tizisintha-sintha kaŵelengedwe kathu. Mbali zotsatilazi zingatithandize: Kuŵelenga mokweza, kapena kutsatila kuŵelengedwa kwa Baibo. M’malo mongotsatila macaputa, tingaŵelenge za munthu winawake wa m’Baibo kapena nkhani inayake. Mwacitsanzo, tingaseŵenzetse kabuku kakuti Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu cigawo 4 kapena cigawo 16, kuti tiŵelenge za Yesu. Tingaŵelenge caputa conse pamene pacokela lemba la tsiku. Tingaŵelengenso mabuku a m’Baibo motsatila ndondomeko yake.

  • Tiziŵelenga n’colinga cakuti timvetsetse. Kuŵelenga caputa imodzi patsiku, kuimvetsetsa, na kuisinkha-sinkha kulibwino kupambana kuŵelenga macaputa ambili tili na colinga cakuti titsilize Baibo. Tingaganizile kumene nkhaniyo inacitikila, na mfundo zofunika m’nkhaniyo. Tingaseŵenzetse mapu na malemba owonjezela okhala m’danga la pakati pa Baibo. Tingayese kufufuza mfundo imodzi imene sitinaimvetsetse. Ngati n’zotheka, tingasinkhe-sinkhe kulingana na nthawi imene tathela poŵelenga Baibo.