Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 25

“Khalanibe Maso”

“Khalanibe Maso”

25:1-12

Ngakhale kuti fanizo la Yesu la anamwali 10 linali kupita kwa otsatila ake odzozedwa, uthenga wake ungagwilenso nchito kwa Akhristu onse. (w15 3/15 mape. 12-16) “Cotelo khalanibe maso cifukwa simukudziŵa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi imwe mungalifotokoze fanizo la Yesu limeneli?

  • Mkwati (vesi 1)—Yesu

  • Anamwali ocenjela ndiponso okonzeka (vesi 2)—Akhristu odzozedwa amene ni okonzeka kukwanilitsa nchito yawo mokhulupilika, na amene amawala ngati zounikila mpaka ku mapeto (Afil. 2:15)

  • Mau ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)—Cizindikilo ca kukhalapo kwa Yesu

  • Anamwali opusa (vesi 8)—Akhristu odzozedwa amene adzapita kukakumana na Mkwati koma sanakhale maso ndiponso sanakhulupilike

  • Anamwali ocenjela anakana kupatsako anzawo mafuta (vesi 9)—Akhristu odzozedwa okhulupilika akadzaikiwa cidindo comaliza, sadzathandizanso aliyense wosakhulupilika

  • “Mkwati Anafika” (vesi 10)—Yesu adzabwela kudzapeleka ciweluzo pamene cisautso cacikulu catsala pang’ono kutha

  • Anamwali ocenjela analoŵa limodzi na mkwati m’nyumba imene munali phwando lacikwati, ndipo citseko cinatsekewa (vesi 10)—Yesu adzasonkhanitsila odzozedwa ake okhulupilika kumwamba, koma osakhulupilika sadzalandila mphoto yawo ya kumwamba