Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki​—Kuthandiza Maphunzilo Athu a Baibo Kukonzekela

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki​—Kuthandiza Maphunzilo Athu a Baibo Kukonzekela

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Ophunzila Baibo akamakonzekela, amakwanitsa kumvetsetsa na kukumbukila zimene timawaphunzitsa. Ngati amvetsetsa na kukumbukila zimene amaphunzila, adzapita patsogolo mwamsanga. Ngakhale pambuyo pa ubatizo, adzafunikabe kukonzekela misonkhano na ulaliki kuti apitilize ‘kukhala maso.’ (Mat. 25:13) Kudziŵa mmene angaphunzilile na kukhala na cizoloŵezi coŵelenga zauzimu, kudzawapindulitsa pa umoyo wawo wonse. Conco, tikangoyamba kuphunzila nawo, tiziwathandiza ophunzila athu kukhala na cizoloŵezi cokonzekela phunzilo.

MMENE TINGACITILE:

  • Khalani citsanzo cabwino. (Aroma 2:21) Konzekelani phunzilo lililonse muli na wophunzila wanu m’maganizo. (km 11/15 3) Muonetseni mmene munacongela m’buku lanu

  • Muzimulimbikitsa kukonzekela. Mukangokhazikitsa phunzilo, uzani wophunzilayo kuti kukonzekela ni mbali ya phunzilo la Baibo. Mufotokozeleninso ubwino wake. Mungamuuze zimene zingam’thandize kupeza nthawi yokonzekela. Ofalitsa ena pocititsa phunzilo la Baibo, amapatsa wophunzila buku lawo locongewa kuti amuthandize kuona ubwino wokonzekela. Muzimuyamikila ngati wakonzekela

  • Muonetseni mmene angakonzekelele. Ofalitsa ena akangokhazikitsa phunzilo, amaseŵenzetsa nthawi yophunzila kuthandiza wophunzila mmene angakonzekelele