Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 20-21

“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenela Kukhala Mtumiki Wanu”

“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenela Kukhala Mtumiki Wanu”

20:28

Alembi na Afarisi onyada anali kukonda kuimilila pamsika kuti anthu awaone na kuwapatsa moni

Alembi na Afarisi onyada anali kufuna kukondweletsa ena, na kuchuka. (Mat. 23:5-7) Koma Yesu anali wosiyana nawo. “Mwana wa munthu sanabwele kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila.” (Mat. 20:28) Pamene ticita mautumiki osiyana-siyana, kodi colinga cathu n’cakuti tichuke na kutamandidwa? Ngati tifuna kukhala wamkulu ngati Yesu, tidzayesetsa kutengela citsanzo cake na kucita zonse zotheka kuti tithandize ena. Nthawi zambili nchito ngati imeneyi sionekela kwa onse. Yehova ndiye amaona. (Mat. 6:1-4) Mtumiki wodzicepetsa amacita izi . . .

  • amathandiza poyeletsa na kukonza Nyumba ya Ufumu

  • amacita zonse zotheka pothandiza okalamba ndi anthu ena

  • amacita zopeleka zothandizila pa nchito za Ufumu