Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makambilano Acitsanzo

Makambilano Acitsanzo

●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi cifunilo ca Mulungu kwa anthu n’ciani?

Lemba: Gen. 1:28

Ulalo: Tidziŵa bwanji kuti Mulungu adzakwanilitsa cifunilo cake pa anthu?

○●○ ULENDO WOBWELELAKO WOYAMBA

Funso: Tidziŵa bwanji kuti Mulungu adzakwanilitsa cifunilo cake pa anthu?

Lemba: Yes. 55:11

Ulalo: Kodi umoyo udzakhala bwanji Mulungu akadzakwanilitsa cifunilo cake?

○○● ULENDO WOBWELELAKO WACIŴILI

Funso: Kodi umoyo udzakhala bwanji Mulungu akadzakwanilitsa cifunilo cake?

Lemba: Sal. 37:10, 11

Ulalo: Kodi tifunika kucita ciani kuti tikapindule na malonjezo a Mulungu?

KAMPENI YOMEMEZA ANTHU KU CIKUMBUTSO (March 23–April 19):

Tikuitanilani ku cocitika cofunika kwambili. Kapepa kanu ka ciitanilo ni aka. Pa Cisanu, April 19, anthu mamiliyoni pa dziko lonse, adzasonkhana kuti acite mwambo wokumbukila imfa ya Yesu Khristu. Kapepa ka ciitanilo aka kaonetsa nthawi na malo kumene msonkhanowu udzacitikile kwathu kuno. Tikuitanilaninso ku nkhani imene idzakambidwa kutatsala wiki imodzi cikumbutso cisanacitike. Mutu wake ni wakuti, “Citani Zonse Zotheka Kuti Mukapeze Moyo Weni-Weni!”

Funso la Ulalo Akaonetsa Cidwi: N’cifukwa ciani Yesu anafa?