Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kalata ya Citsanzo

Kalata ya Citsanzo
  • Seŵenzetsani adresi yanu. Ngati muona kuti si bwino kuseŵenzetsa adresi yanu, mungaseŵenzetse adresi ya Nyumba ya Ufumu, koma mololedwa na akulu. Komabe, SIMUFUNIKA kuseŵenzetsa adresi ya ofesi ya nthambi monga adresi yanu.

  • Lembani dzina la mwininyumbayo ngati mulidziŵa. Mukatelo, munthuyo sangaganize kuti kalatayo ni ya otsatsa malonda.

  • Onetsetsani kuti masipeling’i, ziganizo, komanso zizindikilo zopumila zili bwino. Kalatayo ifunika kukhala yooneka bwino osati yauve. Ngati mwailembela pamanja, ikhale yosavuta kuŵelenga. Mawu a m’kalatayo safunika kukhala opeputsa kapena aulemu kwambili.

Kalata ya citsanzo imene talembayi ionetsa mfundo zimene tafotokoza. Sanailembe n’colinga cakuti muzikopela mawu ake onse mukamalembela munthu wa m’gawo lanu ayi. Lembani kalata yanu mogwilizana n’colinga cake, komanso cikhalidwe ca kumaloko.