Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 1-3

Kodi Ndimwe Munthu Wakuthupi Kapena Wauzimu?

Kodi Ndimwe Munthu Wakuthupi Kapena Wauzimu?

2:14-16

Aliyense wa ife afunika kukulitsa uzimu wake na kupitiliza kukhala munthu wauzimu. (Aef. 4:23, 24) Kuti mupite patsogolo mwauzimu, mufunika kudzidyetsa mwauzimu, kudziikila zolinga zauzimu, komanso kukulitsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala.

Kodi uzimu wanu pali pano uli bwanji mukauyelekezela na mmene unalili caka catha, zaka 10 zapitazo, kapena pamene munabatizika?