Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kulemba Bwino Makalata

Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki—Kulemba Bwino Makalata

N’CIFUKWA CIANI KULI KOFUNIKA? Buku la Akorinto woyamba ni limodzi mwa makalata 14 amene mtumwi Paulo analemba polimbikitsa Akhristu anzake. Kalata imalola munthu kusankha bwino mawu, ndipo woilandila angaiŵelenge mobweleza-bweleza. Makalata ni njila yabwino yolalikilila acibale athu na anzathu. Ni njila inanso yabwino yolalikilila anthu amene n’zovuta kukamba nawo mwacindunji. Mwacitsanzo, munthu angaonetse cidwi koma zimavuta kum’peza panyumba. Mwina ena m’gawo lathu amakhala m’nyumba zansanjika zokhala na citetezo cokhwima, kumageti, kapena amakhala kutali. Ni zinthu ziti zimene muyenela kukumbukila, maka-maka polembela kalata munthu amene simum’dziŵa?

MMENE TINGACITILE:

  • Lembani zimene mukanakamba naye. Kuciyambi kwa kalata dzifotokozeni, ndipo chulani momveka bwino colinga colembela kalatayo. Mwina mungafunse funso kuti munthuyo aganizilepo, kenako mungamuuze za webusaiti yathu. Ndiyeno, muuzeni za Phunzilo la Baibo la pa intaneti, m’fotokozeleni za pulogilamu yathu ya phunzilo la Baibo la panyumba, kapena kumuchulila mitu ina ya nkhani za m’mabuku athu ophunzitsila Baibo. M’kalatayo, mungatsekelemo zofalitsa monga makhadi ongenela pa webusaiti, ciitanilo, kapena mathilakiti.

  • Lembani mwacidule. Kalata yanu sifunika kukhala yaitali kwambili cifukwa woilandilayo angagwe ulesi kuiŵelenga.—Onani kalata yacitsanzo

  • Iŵelengeni kuti mukonze zolakwika. Lembani zooneka bwino komanso zosavuta kuŵelenga. Onetsetsani kuti mwailemba mwaubwenzi, mosamala, ndiponso molimbikitsa. Matikani masitampa okwanila pa emvulupu.