March 25-31
1 AKORINTO 4-6
Nyimbo 123 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Cofufumitsa Cacing’ono Cimafufumitsa Mtanda Wonse”: (10 min.)
1 Akor. 5:1, 2—Mpingo wa ku Korinto unali kulekelela munthu wocita zoipa wosalapa
1 Akor. 5:5-8, 13—Paulo anauza mpingowo kuti ucotse “cofufumitsa” pakati pawo na kupeleka wocita zoipayo kwa Satana (it-2 230, 869-870)
1 Akor. 5:9-11—Mpingo suyenela kuyanjana ndi anthu ocita zoipa amene safuna kulapa (lvs 241, mfundo za kumapeto “Kucotsa Munthu mu Mpingo”)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
1 Akor. 4:9—Kodi atumiki a Mulungu aumunthu ni “coonetsedwa m’bwalo la maseŵela” kwa angelo motani? (w09 5/15 24 ¶16)
1 Akor. 6:3—Kodi Paulo ayenela kuti anatanthauza ciani pamene analemba kuti: “Tidzaweluza angelo”? (it-2 211)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) 1 Akor. 6:1-14 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 11)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) lvs peji 44 (th phunzilo 3)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani na kukambilana vidiyo yoonetsa wofalitsa akuseŵenzetsa vidiyo ya phunzilo 4 m’bulosha ya Uthenga Wabwino, pophunzitsa wophunzila Baibo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 60
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 23 na Pemphelo