Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 4-6

“Cofufumitsa Cacing’ono Cimafufumitsa Mtanda Wonse”

“Cofufumitsa Cacing’ono Cimafufumitsa Mtanda Wonse”

5:1, 2, 5-11, 13

N’cifukwa ciani tingakambe kuti kucotsa munthu mumpingo ni makonzedwe acikondi, popeza cimapweteka mtima?

Kucotsa munthu mu mpingo kumaonetsa kuti . . .

  • timakonda Yehova, komanso timalemekeza dzina lake.—1 Pet. 1:15, 16

  • timakonda mpingo pouteteza ku makhalidwe oipa.—1 Akor. 5:6

  • timakonda wocimwayo cifukwa kumamuthandiza kuzindikila colakwa cake.—Aheb. 12:11

Kodi tingalithandize bwanji banja lacikhristu limene lili na munthu wocotsedwa?