Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo

Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo

Zinthu zooneka zimathandiza munthu kukumbukila na kumvetsetsa zimene anaphunzila. Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, anaseŵenzetsa zinthu zooneka pophunzitsa mfundo zofunika. (Gen. 15:5; Yer. 18:1-6) N’zimenenso Yesu, Mphunzitsi Waluso anacita. (Mat. 18:2-6; 22:19-21) Ndiye cifukwa cake mavidiyo akhala njila yophunzitsila yogwila mtima kwambili m’zaka zaposacedwa. Kodi mavidiyo mumawaseŵenzetsa mokwanila pophunzitsa anthu amene mumaphunzila nawo Baibo?

Pakonzedwa mavidiyo 10, otithandiza pophunzitsa nkhani za m’bulosha yakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. Mitu ya mavidiyo amenewo imagwilizana na mafunso amene ali m’zilembo zakuda kwambili m’bulosha imeneyi. Bulosha ya pa webusaiti ili na malinki otikumbutsa pamene tingatambitse mavidiyowo. Kuwonjezela apo, mavidiyo ena amafotokoza mfundo zowonjezela pa mfundo zopezeka m’zofalitsa zophunzitsila za mu Thuboksi yathu.

Kodi pali nkhani ina ya m’Baibo imene ingakhale yovuta kumvetsetsa pokambilana na wophunzila Baibo? Kodi wophunzila Baibo wanu akukumana na mayeselo enaake? Sakilani mavidiyo pa jw.org® kapena pa JW Broadcasting® amene angamuthandize. Mungacite bwino kutamba imodzi mwa mavidiyo amenewo pamodzi na wophunzilayo, kenako muikambilane.

Mwezi uliwonse kumatuluka mavidiyo atsopano. Pamene muyatamba, ganizilani mmene mungayaseŵenzetsele pophunzitsa ena.