Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 12-14

Kodi Kuonetsa Cikondi Cacikhristu Kumatanthauza Ciani?

Kodi Kuonetsa Cikondi Cacikhristu Kumatanthauza Ciani?

12:10, 17-21

Wina akatilakwila, cikondi cacikhristu cimatithandiza kuti tisabwezele, komanso kuti timucitilebe zinthu mokoma mtima. Paja Baibo imati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse cakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse cakumwa. Pakuti mwa kutelo udzamuunjikila makala a moto pamutu pake.” (Aroma 12:20) Kukoma mtima kumene tingaonetse kwa munthu amene watilakwila, kungam’pangitse kumva kuipa pa zimene waticitila.

Kodi munamvela bwanji pamene munakhumudwitsa munthu wina mosadziŵa, koma iye anayankhabe mokoma mtima?