Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makambilano Acitsanzo

Makambilano Acitsanzo

●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi Yesu anali ndani?

Lemba: Mat. 16:16

Ulalo: N’cifukwa ciani Yesu anafa?

○●○ ULENDO WOBWELELAKO WOYAMBA

Funso: N’cifukwa ciani Yesu anafa?

Lemba: Mt 20:28

Ulalo: Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila nsembe ya dipo la Yesu?

○○● ULENDO WOBWELELAKO WACIŴILI

Funso: Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila nsembe ya dipo la Yesu?

Lemba: Yoh. 17:3

Ulalo: N’ciani cimacitika ku misonkhano ya Mboni za Yehova?

KAMPENI YOMEMEZA ANTHU KU CIKUMBUTSO (March 14–April 7):

“Tabwela kudzakuitanilani ku cocitika capadela ca anthu mamiliyoni ambili. Cocitika cimeneci ni mwambo wokumbukila imfa ya Yesu.” Ndiyeno patsani munthuyo kapepa ka ciitanilo. “Kapepa ka ciitanilo aka kaonetsa nthawi na malo kumene cocitikaci cidzacitikile kwathu kuno. Tikuitanilaninso ku nkhani yapadela imene idzakambiwa pa wikendi yoti cikumbutso cicitika wiki yotsatila.”

Funso la Ulalo Akaonetsa Cidwi: N’cifukwa ciani Yesu anafa?