March 16-22
GENESIS 25-26
Nyimbo 18 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Esau Anagulitsa Udindo Wake Monga Woyamba Kubadwa”: (10 min.)
Gen. 25:27, 28—Esau na Yakobo anali amphundu, koma anali na maumunthu osiyana ndipo anali kucita zinthu zosiyana (it-1 1242)
Gen. 25:29, 30—Esau analola njala na kulema kumucititsa zinthu mopanda nzelu
Gen. 25:31-34—Esau, cifukwa cosayamikila anathamangila kugulitsa ukulu wake kwa Yakobo pofuna cakudya (w19.02 16 ¶11; it-1 835)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 25:31-34—N’cifukwa ciani nkhani ya pa lembali ionetsa kuti kukhala pa mzela wa Mesiya sikunadalile kukhala woyamba kubadwa? (Aheb. 12:16; w17.12 15 ¶5-7)
Gen. 26:7—N’cifukwa ciani Isaki sanakambe zoona zeni-zeni pa cocitikaci? (it-2 245 ¶6)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 26:1-18 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Woyamba: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela mafunso aya: Kodi tingapewe bwanji kucititsa manyazi mwininyumba ngati sadziŵa yankho pa funso imene tam’funsa? Kodi wofalitsa walifotokoza bwanji mogwila mtima lemba la Mateyu 20:28?
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 3)
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. (th phunzilo 15)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muziseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Bulosha Yakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kodi Akufa Ali Mu Mkhalidwe Wabwanji? komanso yakuti N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika? Mukatambitsa vidiyo iliyonse, funsani mafunso aya: Kodi vidiyoyi mungaiseŵenzetse bwanji pophunzila bulosha ya Uthenga Wabwino? (mwb19.03 7) Ni mfundo ziti m’vidiyoyi zimene mwaona kuti n’zothandiza pophunzitsa? Kumbutsani onse kuti bulosha ya Uthenga Wabwino ya pacipangizo ili na malinki a mavidiyo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 108
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 107 na Pemphelo