Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 22-23

“Mulungu . . . Anamuyesa Abulahamu”

“Mulungu . . . Anamuyesa Abulahamu”

22:1, 2, 9-12, 15-18

Kuvutika mtima kumene Abulahamu anamvela pokonzekela kupeleka Isaki nsembe, kumatithandiza kudziŵa mmene Yehova anamvelela pamene anapeleka Mwana Wake Yesu Khristu, monga dipo. (Yoh. 3:16) Kodi mawu a Yehova mu vesi 2 aonetsa bwanji cifundo cake?

Kodi cikondi ca Yehova cimakulimbikitsani kucita ciani?1 Akor. 6:20; 1 Yoh. 4:11