March 23-29
GENESIS 27-28
Nyimbo 10 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yakobo Analandila Madalitso Omuyenelela”: (10 min.)
Gen. 27:6-10—Rabeka anathandiza Yakobo kulandila madalitso a mwana wake woyamba kubadwa (w04 4/15 11 ¶4-5)
Gen. 27:18, 19—Yakobo anapangitsa atate ŵake kuganiza kuti iye ni Esau (w07 10/1 31 ¶2-3)
Gen. 27:27-29—Isaki anapatsa Yakobo madalitso a mwana woyamba kubadwa (it-1 341 ¶6)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 27:46–28:2—Ni phunzilo lanji limene okwatilana angatengepo pa citsanzo ca Isaki na Rabeka? (w06 4/15 6 ¶3-4)
Gen. 28:12, 13—Kodi maloto a Yakobo okhudza “makwelelo” anatanthauza ciani? (w04 1/15 28 ¶6)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 27:1-23 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela mafunso otsatilawa: Kodi wofalitsa waonetsa bwanji kuti anali kumvetsela mwininyumba pamene anali kufotokoza maganizo ake? Kodi wofalitsa waseŵenzetsa bwanji mwaluso zida za mu Thuboksi yathu?
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 6)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) jl phunzilo 17 (th phunzilo 11)