March 30–April 5
GENESIS 29-30
Nyimbo 93 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yakobo Akwatila”: (10 min.)
Gen. 29:18-20—Yakobo anavomela kuseŵenzela Labani zaka 7 kuti akwatile Rakele (w03 10/15 29 ¶6)
Gen. 29:21-26—Labani anapusitsa Yakobo pom’patsa Leya m’malo mwa Rakele (w07 10/1 8-9; it-2 341 ¶3)
Gen. 29:27, 28—Ngakhale kuti Yakobo anakumana na zovuta, anayesetsa kucita zinthu moyenela
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 30:3—N’cifukwa ciani Rakele anakamba kuti ana amene Biliha anabeleka kwa Yakobo ni ake? (it-1 50)
Gen. 30:14, 15—N’cifukwa ciani Rakele ayenela kuti anataya mwayi wokhala na pakati mwa kuusinthanitsa na mandereki? (w04 1/15 28 ¶7)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 30:1-21 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Citani khama pa kuŵelenga na kuphunzitsa (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula, ndiyeno kambilanani phunzilo 16 m’bulosha ya Kuphunzitsa.
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 59 ¶21-22 (th phunzilo 18)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
• “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu”: (10 min.) Nkhani yokambilana yokambidwa na woyang’anila utumiki. Funsani omvetsela mafunso aya: N’cifukwa ciani tifunika kuganizila zosoŵa za anthu osaona? N’kuti kumene tingapeze anthu akhungu? Kodi tingawafikile bwanji? Ni zida ziti zimene tili nazo zothandiza anthu osaona kupita patsogolo mwauzimu?
Zimene Gulu Likukwanilitsa: (5 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa ya March.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 110
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 30 na Pemphelo