Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Anthu ambili akhungu sakhala omasuka kukamba na ŵanthu osaŵadziŵa. Conco pamafunika luso kuti tilalikile anthu amenewa. Yehova amawakonda anthu akhungu. (Lev. 19:14) Tingatengele citsanzo cake mwa kucitapo kanthu kuti tiwathandize mwauzimu.

MMENE TINGACITILE:

  • “Fufuzani” anthu akhungu. (Mat. 10:11) Kodi mudziŵako munthu amene wacibale wake ni wakhungu? Kodi m’gawo lanu muliko masukulu, nyumba zosungilamo anthu osaona amene angafuneko zofalitsa za anthu akhungu?

  • Onetsani mzimu waubwenzi. Kukhala waubwenzi komanso kuonetsa cidwi ceni-ceni kungathandize munthu wakhungu kukhala womasuka. Yesani kuyambitsa makambilano pa nkhani zimene anthu akhungu angacite nazo cidwi

  • Pelekani thandizo la kuuzimu. Pofuna kuthandiza anthu akhungu, gulu lathu lakonza zofalitsa m’mipangidwe yosiyana-siyana. Mungafunse wakhungu kuti afotokoze njila yophunzilila imene afuna. Woyang’anila utumiki afunika kuonetsetsa kuti mtumiki wa mabuku waitanitsa mabuku a anthu akhungu mu mpangidwe umene munthu wakhungu aliyense afuna.