Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 29-30

Yakobo Akwatila

Yakobo Akwatila

29:18-28

Yakobo sanadziŵe mavuto amene anali kudzakumana nawo m’cikwati. Rakele na Leya, anadana koopsa. (Gen. 29:32; 30:1, 8) Koma ngakhale kuti anakumana na mavuto, Yakobo anaona kuti Yehova anali naye. (Gen. 30:29, 30, 43) Ndipo m’kupita kwa nthawi, mbadwa zake zinakhala mtundu wa Isiraeli.—Rute 4:11.

Masiku anonso, anthu amene amasankha kuloŵa m’banja amakumana na mavuto. (1 Akor. 7:28) Ngakhale n’conco, iwo amakhala na mabanja abwino komanso acimwemwe cifukwa codalila Yehova na kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo.—Miy. 3:5, 6; Aef. 5:33.