March 9-15
GENESIS 24
Nyimbo 132 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mkazi wa Isaki”: (10 min.)
Gen. 24:2-4—Abulahamu anatumiza mtumiki wake kukafunila Isaki mkazi pakati pa anthu olambila Yehova (wp16.3 14 ¶3)
Gen. 24:11-15—Mtumiki wa Abulahamu anakumana na Rabeka pa citsime (wp16.3 14 ¶4)
Gen. 24:58, 67—Rabeka anavomela kukwatiwa kwa Isaki (wp16.3 14 ¶6-7)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 24:19, 20—Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene Rabeka anacita zochulidwa m’mavesiwa? (wp16.3 12-13)
Gen. 24:65—N’cifukwa ciani Rabeka anaphimba kumutu kwake? Nanga zimenezi zitiphunzitsa ciani? (wp16.3 15 ¶3)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 24:1-21 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela mafunso otsatilawa: Kodi wofalitsa waseŵenzetsa bwanji mafunso mwaluso? Nanga kodi wofalitsayu wayankha bwanji pamene mwininyumba wapeleka yankho yake ponena za Yesu?
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 1)
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 12)
Kuitanila Anthu ku Cikumbutso: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba aonetse cidwi. Kenako chulani na kukambilana vidiyo yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu. (Koma musaitambitse) (th phunzilo 11)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kampeni Yomemeza Anthu ku Cikumbutso Idzayamba pa Ciŵelu, March 14: (8 min.) Kukambilana. Gaŵilani aliyense m’gulu kapepa koitanila anthu ku cikumbutso na kukambilana zimene zilimo. Tambitsani na kukambilana vidiyo ya ulaliki wacitsanzo. Fotokozani makonzedwe a pa mpingo panu okafolela magawo.
“Kodi Nidzaitanila Ndani?”: (7 min.) Kukambilana.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 107
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 9 na Pemphelo