Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Nidzaitanila Ndani?

Kodi Nidzaitanila Ndani?

Caka ciliconse timayesetsa kuitanila anthu a m’gawo lathu kuti akacite nafe Cikumbutso. Ambili a iwo ni anthu amene sitiŵadziŵa. Tiyenelanso kuitanila anthu amene timaŵadziŵa. Anthu amene amalandila ciitano kucokela kwa anthu amene amaŵadziŵa, kambili amapezeka ku cikumbutso. (yb08 11 ¶3; 14 ¶1) Ni anthu ena ati amene mungaitanile?

  • Acibululu

  • Anzanu a kunchito kapena a kusukulu

  • Maneba

  • Anthu amene munapangako maulendo obwelelako na maphunzilo a Baibo akale komanso atsopano

Kuwonjezela apo, akulu adzaitanila anthu ozilala. Nanga bwanji ngati munthu amene mudziŵana naye sakhala m’dela lanu? Mungafufuze nthawi na malo kumene Cikumbutso cidzacitikila kumene munthuyo akhala, mwa kutinika pa mbali yakuti ZOKHUDZA IFE imene ili pamwamba pa peji yoyamba pa jw.org. Kenako sankhani polemba kuti ““Cikumbutso.” Pokonzekela cikumbutso ca caka cino, ganizilani anthu amene mungaitanile, ndipo mukawapatsedi ciitanilo.