April 12-18
NUMERI 20-21
Nyimbo 114 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khalanibe Ofatsa Mukapanikizika na Mayeso”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu (Mph. 10)
Num. 20:23-27—Tiphunzilapo ciani tikaona mmene Aroni anacitila zinthu atapatsidwa uphungu komanso mmene Yehova anamuonela ngakhale kuti analakwa? (w14 6/15 26 ¶12)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Num. 20:1-13 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 12)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani cofalitsa ca mu Thuboksi yathu. (th phunzilo 3)
Nkhani: (Mph. 5) g 1/15 9—Mutu: Kodi Ningalamulile Bwanji Mtima Wanga? (th phunzilo 16)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muzikamba Mawu Olimbikitsa kwa Ena: (Mph. 7) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso aya: Kodi kukamba mawu osalimbikitsa kapena kudandaula kumakhudza bwanji anthu ena? N’ciani cinathandiza m’bale amene taona mu vidiyo kusintha khalidwe lake?
Musagonje Anzanu Pokunyengelelani!: (Mph. 8) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi ya zithunzi zojambula pamanja. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso aya: Kodi anthu ambili anzawo amawanyengelela kucita ciani? Kodi pa Ekisodo 23:2 pali malangizo otani? Ni njila zinayi ziti zimene zingatithandize ngati anzathu amatinyengelela kucita zoipa?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30.) lfb phunzilo 31
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 10 na Pemphelo